Kusiyana Kwa Baibulo Ndi Qur'an

BaibuloQur'an
Limanena kuti Mulungu ndi m’modzi, komanso utatu wa Umulungu, (Yesaya 43:10; Mateyu 28:19; 2 Akolinto 13:14).Imanena kuti Mulungu ndi m’modzi (5:73; 112:1-4), koma imakana za utatu wa Umulungu (5:73).
Limanena kuti Yesu ndi Mulungu m’thupi (Akolose 2:9).Imanena kuti Yesu si mwana wa Mulungu (5:17, 75).
Limanena kuti Yesu anapachikidwa pa mtanda (1 Petro 2:24).Imanena kuti Yesu sanapachikidwe pa mtanda (4:157).
Limanena kuti Yesu anuka kwa akufa (Yohane 2:19).Imanena kuti Yesu sanapachikidwe pa mtanda (4:157).
Limanena kuti Yesu anali mwana wa Mulungu (Maliko 1:1).Imanena kuti sanali mwana wa Mulungu (9:30).
Limanena kuti Mzimu Woyera ndi wachitatu mu Umulungu ndipo amachitira umboni za Yesu (Yohani 14:26; 15:26).Imanena kuti Gabriel ndi M’ngelo (2:97; 16:102).
Limanena kuti munthu adzapulumutsidwa ndi chisomo kupyolera m’chikhulupiliro (Aefeso 2:8,9).Imanena kuti chipulumutso tidzachipeza pochita zachifundo komanso ntchito zathu (3:135; 7:8-9; 21:47; 49:14; 66:8-9).
Limanena kuti Satana ndi m’ngelo wakugwa (wochimwira Mulungu) Yesaya 14:12-15)Imanena kuti Satana si m’ngelo wakugwa(wochimwa) komatu Jinn wakugwa(wochimwa) (2:34; 7:12; 15:27; 55:15).
Limanena kuti munthu ndi wochimwa(wakugwa mu uchimo), (Aroma 3:23).Imanena kuti munthu ndi wosachimwa (wabwino).
Limanena kuti ophunzira a Yesu anali akhristu (Machitidwe 11:26).Imannena kuti ophunzira a Yesu anali anadzitcha okha Asilamu (15:111).
Limanena kuti poyamba chipembedzo chinali kuchitika pa Sabata (Exsodo 20). Ndipo kenako tsiku loyamba la Sabata(la Mulungu) (Aroma 14:5-6; Machitidwe 20:7; 1 Akolinto 16:1-2).Imanena kuti Asilamu ayenera kepembedza la chisanu (62:9).
Limanena kuti m’Baibulo munalembedwa zizizwitsa zambiri.Mulibe zozizwizitsa kupaturapo kuti Quraniyo ndi bukhu lozizwitsa.
Limanena kuti m’Baibulo muli maulosi ambiri.Mulibe ulosi.

NB. Ndidzakhala ndikukupatsirani zinanso zikapezeka.