Mbiri Ya Chiyambi Cha Chiislamu

Taonani m’mene chiyambi cha Chisilamu chimakhudzidwira ndi nkhondo. Kuyambira m’chaka cha 623 mpaka 777, mpata wa zaka 154 (zaka zana limodzi ndi makumi asanu ndi zinai), padachitika nkhondo za Chisilamu zokwana 83 (makumi asanu ndi atatu ndi zitatu). Izitu ndi zomwe zangolembedwa pa masamba ano. Kodi Chisilamu ndi chipembedzo cha mtendere? Asilamu amatitu inde ndi chipembedzo cha mtendere. Komatu zinthu zinali motere….

 • 570-Kubadwa kwa Muhammad ku Makka pakati pa mtundu wa chiQuraish.
 • 577-Kumwalira kwa mayi a Muhammad.
 • 580-Kumwalira kwa Abdul Muttalib, agogo a Muhammad.
 • 583-Ulendo wake woyamba wagulu la malonda wopita ku Syria.
 • 595-Muhammad anakwatira Khadijah mkazi wa masiye yemwe anali wa zaka zambiri kuposa iye.
 • 595-Ulendo wake wachiwiri wa ku Syria.
 • 598-Kubadwa kwa mwana wake wa mamuna Qasim.
 • 600-Kubadwa kwa mwana wake wa mkazi  Zainab.
 • 603-Kubadwa kwa mwana wake wa mkazi Um-e-Kalthum.
 • 604-Kubadwa kwa mwana wake wa mkazi Ruquyya.
 • 604-Kuika kwa mwala wakuda mu Ka’aba.
 • 605- Kubadwa kwa mwana wake wa mkazi Fatima.
 • 610-Muhammad pamene anali m’phanga la phiri la Hira anamva ngelo Gabriel akumuuza kuti Allah ndi Mulungu m’mmodzi woona.
 • 613-Kulalikira koyamba kwa Muhammad pa phiri la Hira ndipo anthu ena anamutsatira.
 • 615-Asilamu anayamba kudzunzidwa ndi a Quraish.
 • 619-Muhammad anakwatira Sau’da ndi Aisha.
 • 620-Kukhazikitsidwa kwa Msanamira zisanu za chipembedzo Chisilamu.
 • 622-Muhammad asamunika kuchoka ku Mecca ndi kupita Medina komwe kunkatchedwanso ku Yathrib.
 • 623-Nkhondo ya Wadda.
 • 623-NkhondO ya Safwan.
 • 623-Nkhondo ya Dul-Ashir.
 • 624-Muhammad ndi omutsatira ake anayamba kuchitira uchifwamba magulu amalonda kuti apeze ndalama zoyendetsera gulu lawo.
 • 624-Zakat inakhala lamulo.
 • 624-Nkhondo ya Badr.
 • 624-Nkhondo ya Bani-Salim.
 • 624-Nkhondo ya Eid-ul-Fitr ndi Zakat-ul-Fitr.
 • 624-Nkhondo ya Bani Qainuq’.
 • 624-Nkhondo ya Sawiq.
 • 624- Nkhondo ya Ghatfan.
 • 624- Nkhondo ya Bahran.
 • 625-Nkhondo ya Uhud; Asilamu 70 (makumi asanu ndi awiri) anaphedwa.
 • 625-Nkhondo ya Humra-ul-Asad.
 • 625-Nkhondo ya Banu Nudair.
 • 625-Nkhondo ya Dhatur-Riqa.
 • 626-Nkhondo ya Badru-Ukhra.
 • 626-Nkhondo ya Dumatul-Jandal.
 • 626-Nkhondo ya Banu Mustalaq Nikah.
 • 627-Nkhondo ya Trench.
 • 627-Nkhondo ya Ahzab.
 • 627-Nkhondo ya Bani Quraiza.
 • 627-Nkhondo ya Bani Lahyan.
 • 627-Nkhondo ya Ghaiba.
 • 627- Nkhondo ya Khaibar.
 • 628-Muhammad anapangana pangano la mgirizano ndi a Quraish.
 • 630-Muhammad anagonjetsa ndi kulanda mzinda wa Mecca.
 • 630-Nkhondo ya Hunsin.
 • 630-Nkhondo ya Tabuk.
 • 632-Kumwalira kwa Muhammad.
 • 632-Abu-Bakr, mpongozi wa Muhammad pamodzi ndi Umar anayamba nkhondo yokakamiza kuti Chisilamu chikhazikitsidwe m’madera onse a Aluya(Arabia).
 • 633-Nkhondo pamalo otchedwa Oman.
 • 633-Nkhondo pamalo otchedwa Hadramaut.
 • 633-Nkhondo ya Kazima.
 • 633-Nkhondo ya Walaja.
 • 633-Nkhondo ya Ulleis.
 • 633-Nkhondo ya Anbar.
 • 634-Nkhondo ya Basra.
 • 634-Nkhondo ya Damascus.
 • 634-Nkhondo ya Ajnadin.
 • 634-Kumwalira kwa Hadrat Abu Bakrn ndipo Hadrat Umar  anakhala mtsogoleri.
 • 634- Nkhondo ya Namaraq.
 • 634- Nkhondo ya Saqatia.
 • 634-Nkhondo ya Bridge.
 • 635-Nkhondo ya Buwaib.
 • 635-Kugonjetsedwa kwa Mzinda wa Damascus.
 • 635-Nkhondo ya Fahl.
 • 636-Nkhondo ya Yermuk.
 • 636-Nkhondo ya Qadsiyia.
 • 636-Kugonjetsedwa kwa Madain.
 • 637-Nkhondo ya Jalula.
 • 638-Nkhondo ya Yarmouk.
 • 638-Asilamu agonjetsedwa Aroma ndi kulowa mu Yerusamu.
 • 638-Kugonjetsedwa kwa Jazirah.
 • 639-Kugonjetsedwa kwa Khuizistan and kulowanso m’dziko la Egypt.
 • 641-Nkhondo ya Nihawand.
 • 642-Nkhondo ya Rayy ku Persia.
 • 643-Kugonjetsedwa kwa Ararbaijan.
 • 644- Kugonjetsedwa kwa Fars.
 • 644- Kugonjetsedwa kwa Kharan.
 • 644-Umar anaphedwa ndipo Uthman anakhala mtsogoleri.
 • 647-Kugonjetsedwa kwa chilumba cha Cyprus.
 • 648-Kuyamba kwa nkhondo yolimbana ndi Byzantines.
 • 651-Nkhondo ya pamadzi ndi Byzantines.
 • 654-Chisilamu chifalikira  ku mpoto kwa Africa.
 • 656-Uthman anaphedwa ndipo Ali anakhala mtsogoleri.
 • 658-Nkhondo ya Nahrawan.
 • 659-Kugonjetsedwa kwa Egypt.
 • 661-Ali anaphedwa.
 • 662-Dziko la Egypt linakhala pansi pa ulamuliro wa Chisilamu.
 • 666-Sicily analandidwa ndi Asilamu.
 • 677- Constantinople anazunguliridwa ndi Asilamu.
 • 687-Nkhondo ya Kufa.
 • 691- Nkhondo ya Deir ul Jaliq.
 • 700- ChiSufism chinakhazikika ngati gulu lina la Chisilamu.
 • 700-Nkhondo ku Mpoto kwa Africa.
 • 702- Nkhondo ya Deir ul Jamira.
 • 711-Asilamu analanda Gibraltar.
 • 711-Kugonjetsedwa kwa Spain.
 • 713- Kugonjetsedwa kwa Multan.
 • 716- Kugonjetsedwa kwa Constantinople.
 • 732- Nkhondo ya Tours ku France.
 • 740- Nkhondo ya Nobles.
 • 741- Nkhondo ya Bagdoura ku Mpoto kwa Africa.
 • 744- Nkhondo ya Ain al Jurr.
 • 746-Nkhondo ya Rupar Thutha.
 • 748-Nkhondo ya Rayy.
 • 749-Nkhondo ya Isfahan.
 • 749- Nkhondo ya Nihawand.
 • 750-Nkhondo ya Zab.
 • 772-Nkhondo ya Janbi ku Mpoto kwa Africa.
 • 777-Nkhondo ya Saragossa ku Spain.

 

Mabuku:

 • Miller, William M., A Christian’s Response to Islam, Presbyterian and Reformed Publishing, Phillipsburg, New Jersey, 1976.
 • Geisler, Norma, Baker Encyclopaedia of Christian Apologetics, Grand Rapids, Michigan, Baker Books, 1999.
 • Glasse, Cyril, The Concise Encyclopaedia of Islam, Harper & Row, Publishers, INC. San Fransisco, 1989.
 • Morey, Robert, The Islamic Invasion, Harvest House Publishers, Eugene Oregon, 1992.
 
 

About The Author

Matt Slick is the President and Founder of the Christian Apologetics and Research Ministry.